Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Josebu-basebete Mtakemoni, mkuru wa akazembe; ameneyu ndiye Adino M-ezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.