35. Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;Kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.
36. Ndiponso munandipatsa cikopa ca cipulumutso canu;Ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.
37. Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,Ndi mapazi anga sanaterereka.
38. Ndinapitikitsa adani anga, ndi kuwaononga;Ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha.
39. Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka,Inde anagwa pansi pa mapazi anga.
40. Pakuti Inu munandimanga m'cuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; Munandigonjetsera akundiukira.
41. Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,Kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.
42. Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;Ngakhale kwa Yehova, koma iye sanawayankha.
43. Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati pfumbi la padziko,Ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala.
44. Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;Munandisunga ndikhale mutu wa amitundu;Anthu amene sindinawadziwa adzanditsumikira ine.
45. Alendo adzandigonjera ine,Pakumva za ine, adzandimbera pomwepo.
46. Alendo adzafota,Nadzabwera ndi kunthunthumira oturuka mokwiririka mwao.
47. Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;Ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la cipulumutso canga;
48. Inde Mulungu wakundibwezera cilango ine,Ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.
49. Amene anditurutsa kwa adani anga;Inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira;Mundipulumutsa kwa munthu waciwawa.
50. Cifukwa cace ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu,Ndipo ndidzayimba zolemekeza dzina lanu.