Naika mafupa a Sauli ndi Jonatani mwana wace ku dziko la Benjamini m'Zela, m'manda a Kisi atate wace; nacita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pace Mulungu anapembedzeka za dzikolo.