Ndipo Abineri ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zace. Koma Asaheli anakana kupambuka pakumtsata iye.