Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzace, nagwaza ndi lupanga lace m'nthiti mwa mnzaceo Comweco anagwa limodzi; cifukwa cace malo aja anachedwa Dera la Mipeni la ku Gibeoni.