Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mudzi wanga ku manda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Cimamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumcitire cimene cikukomerani.