Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'cidzenje cacikuru kunkhalangoko; naunjika pamwamba pace mulu waukuru ndithu wamiyala; ndipo Aisrayeli onse anathawa yense ku hema wace.