Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anacoka msanga onse awiri, nafika ku nyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali naco citsime pabwalo pace; ndipo anatsikira m'menemo.