Cifukwa cace tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti, Musagona usiku uno pa madooko a kucipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.