Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali: nao osenga nkhosa zace ku Baalahazore pafupi pa Efraimu; ndipo Abisalomu anaitana ana amuna onse a mfumu.