Ndipo Abisalomu mlongo wace ananena nave, Kodi mlongo wako Arononi anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale cete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usabvutika ndi cinthuci. Comweco Tamara anakhala wounguruma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wace.