Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumiza anyamata ace kwa inu, kuti ayang'ane mudziwo ndi kuuzonda ndi kuupasula?