Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda pa phiri la Giliboa, ndinaona, Sauli alikuyedzamira nthungo yace, ndi magareta ndi apakavalo anamyandikiza.