Ndi mfumu ya Aigupto anamlonga Eliyakimu mng'ono wace mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu, nasintha dzina lace likhale Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yehoahazi mkuru wace, namuka naye ku Aigupto.