Caka coyamba tsono ca Koresi mfumu ya Perisiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Koresi mfumu ya Perisiya, kuti abukitse mau m'ufumu wace wonse, nawalembenso, ndi kuti,