Ndipo Yosiya anapatsa ana a anthu zoweta, ana a nkhosa ndi a mbuzi zikhale zonsezo za nsembe za Paskha kwa ali yense anali komweko; zinafikira zikwi makumi atatu, ndi ng'ombe zikwi zitatu, ndizo zotapa pa cuma ca mfumu.