Yosiya nacotsa zonyansa zonse m'maiko onse okhala a ana a Israyeli, natumikiritsa onse opezeka m'lsrayeli, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ace onse iwo sanapambuka kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao.