Ndi anthu onse anamuka ku nyumba ya Baala, naipasula, naphwanya maguwa ace a nsembe, ndi mafano ace; namupha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe.