Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu cokoma ngati m'kamwa m'modzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene cokoma.