Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ocokera m'mafuko onse a Israyeli, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israyeli, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe.