Naturutsa cifanizoco m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nacitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nacipera cikhale pfumbi, naliwaza pfumbi lace pa manda a ana a anthu.