Ndipo Farao-Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wace, nasanduliza dzina lace likhale Yoyakimu; koma anapita naye Yoahazi, nafika iye m'Aigupto, nafa komweko.