Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, nelidzakuciritsa, tsiku lacitatu udzakwera kumka ku nyumba ya Yehova.