15. Nati iye, Anaona ciani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pacuma canga kosawaonetsa.
16. Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Tamverani mau a Yehova.
17. Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kumka ku Babulo, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.
18. Nadzatenga ena a ana ako oturuka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'cinyumba ca mfumu ya Babulo.
19. Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi coonaeli zikakhala masiku anga?
20. Macitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yace yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mcera, nautengera mudzi madzi, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
21. Nagona Hezekiya ndi makolo ace; nakhala mfumu m'malo mwace Manase mwana wace.