Koma anamuumiriza kufikira anacita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza.