Sunamva kodi kuti Ine ndinacicita kale lomwe, ndi kucipanga masiku akalekale? tsopano ndacifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula imidzi yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.