Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kumka ku nyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.