Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zobvala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.