29. Koma a mtundu uli wonse anapanga milungu yao yao, naiika m'nyumba za misanje adazimanga Asamariya, a mtundu uli wonse m'midzi mwao mokhala iwo.
30. Ndipo anthu a Babulo anapanga Sukoti Bemoti, ndi anthu a Kuta anapanga Nerigali, ndi anthu a Hamati anapanga Asima,
31. ndi Aava anapanga Nibazi ndi Tarataka; ndi a Sefaravaimu anawatentha ana ao m'moto kwa Adrameleki, ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.
32. Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m'nyumba za misanje.
33. Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawacotsako.
34. Mpaka lero lino acita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sacita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena cilamulo, kapena coikika adacilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamucha Israyeli,
35. ndiwo amene Yehova adapangana nao, nawalamulira, ndi kuti, Musamaopa milungu yina, kapena kuigwadira, kapena kuitumikira, kapena kuiphera nsembe;
36. koma Yehova amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;
37. ndi malemba, ndimaweruzo, ndi cilamulo, ndi coikika anakulemberani muzisamalira kuzicita masiku onse, nimusamaopa milungu: yina;
38. ndi cipangano ndinacicita nanu musamaciiwala, kapena kuopa milungu yina iai;
39. koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse.
40. Koma sanamvera, nacita monga mwa mwambo wao woyamba.