Ndipo pamene Samueli analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisrayeli; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukuru pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisrayeli.