Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, cifukwa ca cofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda.