Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene.