Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samueli. Ndipo Samueli anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitana, mwana wanga; kagone.