Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe cimene mnyamata wanu adzacita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Cifukwa cace ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.