Ndipo Davide sadasunga wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ace ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.