Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 27:10-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo Akisi anati, Wapooyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameli, ndi a kumwera kwa Akeni.

11. Ndipo Davide sadasunga wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ace ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.

12. Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israyeli, cifukwa cace iye adzakhala mnyamata wanga cikhalire.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 27