Comweco Davide ndi anthu ace anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri Motero Davide analanditsa okhala m'Keila.