Ndipo Davide anakhala m'cipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'cipululu ca Zifi. Ndipo Sauli anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereka m'dzanja lace.