Cifukwa cace ucitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamcititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli coipa ciri conse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?