Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Jonatani asadziwe ici, kuti angamve cisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazilimodzi.