nati, Ndiloleni, ndimuke; cifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mudzimo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndicoke, ndikaone abale anga. Cifukwa ca ici safika ku gome la mfumu.