Ndipo kunali tsiku laciwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pace; ndipo Sauli anati kwa Jonatani mwana wace, Mwana wa Jese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?