Ndipo Davide anathawa ku Nayoti m'Rama, nadzanena pamaso pa Jonatani, Ndacitanji ine? kuipa kwanga kuli kotani? ndi chimo langa la pamaso pa atate wanu ndi ciani, kuti amafuna moyo wanga?