Ndipo Sauli analamulira anyamata ace, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ace onse akukondani; cifukwa cace tsono, khalani mkamwini wa mfumu.