Ndipo anthu a Israyeli ndi Ayuda ananyamuka, napfuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka ufika kucigwako, ndi ku zipata za Ekroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa pa njira ya ku Saraimu, kufikira ku Gad ndi ku Ekroni.