Ndipo Samueli sanadzanso kudzaona Sauli kufikira tsiku la imfa yace; koma Samueli analira cifukwa ca Sauli; ndipo Yehova anali ndi cisoni kuti anamlonga Sauli mfumu ya Israyeli.