Kundicititsa cisoni kuti ndinaika Sauli akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanacita malamulo anga, Ndipo Samueli anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.