Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Yehova ananditumiza ine kukudzozani mukhale mfumu ya anthu ace Aisrayeli; cifukwa cace tsono mumvere kunena kwa mau a Yehova.