Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uci anacuruka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lace pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo.