Ndipo a ku kabomawo anayankha Jonatani ndi wonyamula zida zace, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Jonatani anauza wonyamula zida zace, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israyeli.